Zikomo Lyrics


VERSE 1
Pomwe zinthu zafikapa ndatutumuka
Sindinali kuyembekeza zingakhale chonchi
Ndisaname mbuye wanga mwandilemekeza
Zikomo
Njira yanga mwaidzadza ndi dangalira
Mtima wanga mwawutulutsa mu m'dima
Moyo wanga mwaudzadza ndi madalitso
Zikomo ooh

CHORUS
Zikomo Zikomo Zikomo
Zikomo Allah zikomo Allah zikomo
Pa zonse mwandichitira (zikomo)
Mwanditulutsa mu m'dima (zikomo)
MwandiWongolera njira
ooh zikomo
Mwanditulutsa mu m'dima
MwandiWongolera njira ooh
zikomo oooh
VERSE 2
Sindifuna kukhara wodzitamandira
Poti nthawi iliyonse inu mutafuna
Zonsezi ndilinazo mukhoza kulanda
ooh
Ndikudziwa mabvuto sangatheretu
Komabe sindingaleke kuyamika
Chifukwa mumamva kulira kwanga ooh

CHORUS
Zikomo Allah zikomo Allah zikomo Allah zikomo x2
Pazonse mwandichitira (zikomo)
Mwanditulutsa mu m'dima (zikomo)
Mwandiwongolera njira (zikomo)
ooh zikomo
Pazonse mwandichitira (zikomo)
Mwandiwongolera njira (zikomo)
Mwanditulutsa mum'dima (zikomo)
ooh
Zikomo.

To download the song Zikomo, click here

Comments

Popular posts from this blog

Zikomo

Biography