Tidzapambana lyrics
VERSE 1
Oh Malawi dziko lathu lokongora
La mkakanso ndi uchi chilengedwe chapamwamba
Oh Malawi dziko lathu lokongora
La mkakanso ndi uchi chilengedwe chapamwamba
Adalilenga Mulungu natiikamo tonsefe
Inu ndi achimwene anga awo ndi achemwali anga
Tonse ndife banja limodzi olo ndili wa alubino
Ndilinso ndikuthekera aliyense ndiwofunika
CHORUS
Ife tatsamira mwa Mulungu sititaya chiyembekezo
Timadzikhulupilira ndife anthu ofunika
Ndi mphamvu ya Mulungu Ifeyo tidzapambana
VERSE 2
Zimatheka munthu yemwe umam'nyoza
Kudzakugwira pamkono tsiku lina utabvutika
Usam'nyoze munthu mzako chifukwa choti ndi wa alubino
Ine tsiku ndi tsiku ndikamakhara ndimakhara ndi zokhumba
Khumbo langa lalikuru ndilo kuwakonda anthu onse

M'mene ndimadzikondera ndekha nanunso bwanji mutatero
REPEAT CHORUS x 2
Usataye chiyembekezo iwe mzanga wa alubino
Kwa onse oferedwa chonde lekani kulira
Musataye mtima Mulungu akuona
OUTRO
Ooh yeeh ooh yeeh
Poti zolengedwa zonse ndi za Mulungu
Tonsefe ndi ake amatikonda chmodzimodzi.

To download the song Tidzapambana, click here
Comments
Post a Comment