Tiganizenso lyrics

VERSE 1
Mbuye wazolengedwa anaika lamulo
kuti anthu tonsefe timupembedze iye yekha
ndimitima yathu yonse koma ife tikukanira aah

CHORUS
Tsono kupempha chikhululuko ndipomwe tili moyo
Tikadzangoti tamwalira sitidzatha kulapa
Kudzatsale nkuweruzidwa tsiku loikikalo
chilango chauchimo nchowawa chonde tiganizenso

VERSE 2
Timadzinyenga tokha kuti tamkhulupilira
pomwe tikukanira adzitumiki ake ena
ndikumavomera ena chikhulupiliro chanji chotero

CHORUS
Ndiye kupempha chikhululuko ndipomwe tili moyo
Tikadzangoti tamwalira sitidzatha kulapa
Chidzatsale ndi chiweruzo tsiku likubwelaralo
Ngati sitifuna kulira tiganizenso

Tsono lero tivomereze kuti Mulungu ndi m'modzi
yemwe analenga tonsefe ndizopezeka zonse
tisamphatikizenso ndichilichonse pomupembedza
tisapembezenso zolengedwa zake koma Olengayo

Uuu yeeeee uu yee uuyeeuyee
Mulungu wachifundo chambiri ndinso wachisomo
Mutitsegule ife masowa natisonyeza njira
palibe ndithu m'modzi mwa ife amafuna kulangidwa
tonsefe tikufuna tidzalowe ku paradizo wanu

To download the song Tiganizenso, click here

Comments

Popular posts from this blog

Zikomo

Biography